A.1 Ulimi wogwirizana ndi nyengo
Ndondomekozi zimapereka njira za ulimi woyenera - umene umathandizira potukula ubwino wa dothi potukula maonekedwe a dothi, kapangidwe ka mankhwala ka dothi, ndi chilengedwe cha dothilo. Dothi labwino limapereka zokolola zambiri. Ndondomekozi zimathandizira popewa kukokoloka kwa nthaka ndi kuthamanga kwa madzi pa nthaka poonjezera kulowa kwa madzi m’nthaka ndi kasungidwe ka madzi m’ nthakamo. Ulimi wogwirizana ndi nyengo umakhudza ulimi wa mleranthaka ndi mbwezerachilengedwe kapena kuti ulimi wa chilengedwe.