B.3 Kulowa pansi kwa madzi

Ndondomekozi zikulongosola mmene kalowedwe pansi ka madzi a mvula kangaonjezeredwere, zimene zingakweze kapezekedwe ka madzi osungidwa mu mizu komanso pansi pa nthaka. Kuonjezereka kwa madzi mu mizu kumachepetsa kudalira madzi othirira, ndipo kumaonjezera mwayi wobzala m’nyengo ya chilimwe. Kuchuluka kwa madzi pansi pa nthaka kumachititsa kuti akasupe akhale ndi madzi komanso kumakweza kayendedwe ka madzi pa nthaka komanso mulingo wa madzi muzitsime zoyandikira.