D.4 Kasamalidwe ka zomera zachilendo zowononga chilengedwe
Ndondomeko izi zikufotokoza mfundo zophunzitsa anthu pa njira zomwe angatsate posamalira zomera zachilendo komanso zowononga zachilengedwe. Zomera zachilendo zowononga zachilengedwe zimaopseza zinthu zopezeka m’madzi komanso kapezekedwe ka madzi. Poyng’anira zomera zimenezi ndi kupewa kuti zisapitirire kufalikira, zomerazi zitha kukhala zofunikira ndi kulowanso mmalo mwa zomera za m’madera athu zomwe panopa zikutha mofulumira.