E.3 Njira Zolimbana ndi Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi
Njira izi zikupereka uphungu pa momwe tingachitire pa ngozi zosiyanasiyana. Ndondomeko izi zaperekedwa pofun kuthana ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi, zoyika miyoyo ya anthu pa chiopsezo (monga madzi osefukira), komanso ngozi zotenga nthawi yayitali (monga chilala). Njira zofuna kuyambitsa dongosolo lodziwitsiratu anthu za ngozi yomwe ikuyembekezereka kuchitika zafotokozedwa. Ndondomeko izi kwenikweni zikufotokoza za zinthu zomwe anthu angazichitedi zomwe zingathandize kuchepetsa mavuto akudza kamba ka ngozizi pa miyoyo ya anthuwo.