A - Sustainable Land Management
Kukokoloka kwa nthaka, kudula mitengo mosasamala, njira zosayenera za ulimi, kutha kwa chonde m’nthaka, kusathana ndi kuthamanga kwa madzi a mvula pa nthaka ndi kukumbika kwa malo zimagugitsa komanso kuonongetsa malo m’Malawi muno. Kuti tichepetse kuonongeka kwa malo, tithane ndi kuonongeka kwa amalo komanso kugwiritsa ntchito malo moyenera, mutu uwu wapereka ndondomeko zochitira izi.
Chimodzi mwa zachilengedwe chomwe ndi chofunikira kwambiri ndi dothi.Dothi la chonde komanso labwino limapereka zokolola zambiri; pamene dothi loguga kapena loonongeka limapereka zokolola zochepa komanso zosadalirika.Dothi labwino limakhala ndi muyeso wabwino woti mizu ilowepo, imakhala ndi chonde, looneka bwino, limakhala ndikuthekera kosunga za moyo zambiri, komanso madzi ndipo zonsezi ndi zolumikizana. Poonetsetsa kuti dothi likhalebe labwino komanso la chonde pakufunikira njira za kasamaliridwe zosiyanasiyana monga: njira ya ulimi ya mbwezerachilengedwe, kusamalira malo odyetsera ziweto, kusamalira chonde m’nthaka, njira zopewera kukokoloka kwa nthaka, kusamalira malo okumbika, kusamalira m’mbali mwa mitsinje. Kukwaniritsa njirazi kungachepetse kuonongeka kwa chonde (makamaka kudzera mu kukokoloka kwa nthaka) ndi kuguga kwa nthaka (zomwe zimachepetsa chonde komanso kuchepetsa kasungidwe ka madzi m’dothi); kusintha kwa nyengo kungakhale kusaopsa, kulephera kwa mbewu kuchitabwino kungachepe, ndipo dothi mu gwero lonse la mtsinje lingatetezeke ndi kusungika.
B - Water Harvesting and Storage
Madzi ndi ofunika kwambiri pa moyo komanso ulimi. Zinthu ziwiri zomwe zimakhudza madzi ndi: kapezedwe ka madzi ndi kasamalilidwe ka madziwo. Kapezedwe ka madzi katha kukwezedwa kudzera mukusunga madzi pa banja kapena mudzi.Kapezedwe ka madzi kamakwezedwanso kudzera mukugwiritsa ntchito madzi mosamala kuti asathe mwamsanga; izi zimatheka kudzera mukugwiritsa ntchito madziwo kangapo.
Ndondomekozi zikulongosola njira za kagwiritsidwe ntchito ka madzi mosamala komanso kugwiritsa ntchito kangapo, kusonkhanitsa madzi a mvula ndi kasungidwe kake, kalowedwe ka madzi pansi pa nthaka, madamu ang’onoang’ono, ndi ulimi wothirira wa m’masikimu. Kapezedwe ka madzi, kangapangitse kuti madzi azisamalidwa moyenera, zomwe ndizothandiza kwa anthu onse komanso pa gwero la madzilo.
C - Household Management
Pofuna kuonetsetsa kuti ntchito zosamalira komwe anthu amachokera komanso ulimi wamakono ukuchitikadi, n’kofunika kuti ntchito zochitika pakhomo, kumunda ndiponso m’mudzi nazonso zizikhala zothandiza komanso zabwino.
Ntchitozi ndi monga kumanga nkhokwe zamakono, kusamalira mijigo, nazale za mbande, mitengo yobzala mwampanda, zaukhondo, njira zina zopezera moto, kugwiritsa ntchito moto moyenera, ndi kutaya zinyatsi mwadongosolo. (Check energy)
D - Natural Resource Management
Anthu amadalira zachilengedwe kuti apeze ndalama zowathandiza pa moyo wawo. Kugwiritsa ntchito zachilengedwe mosasamala kumachittsa kuti izozi zitheretu. Choncho zachilengedwe zifunika kuzisamalira ndi kuzigwiritsa ntchito mosinira kuti phindu lomwe timapeza ku zachilengedwezo likhale lochuluka kwinaku zikugwira ntchito zake. Nkhalango zachilengedwe, malo osodza nsomba ndi madambo ndi zinthu zofunika kwambiri ndipo ziyenera kusamalidwa mosalekeza; chimodzimodzinso zomera zachilendo zitha kukhala zaphindu koma zifunika kuziyang’anira bwino popewa kuti zingafalikire mopanda dongosolo.
Gawo lino likuunikira pa momwe tingasamalire ndi kugwiritsa ntchito bwino zachilengedwezi.
E - Disaster Preparedness
Mavuto ogwa mwadzidzidzi ndi ngozi zitha kuchitika pena paliponse komanso nthawi ina iliyonse. Komabe m’madera momwe zachilengedwe zaonongeka kapena momwe malibe dongosolo lokhudza mavuto ogwa mwadzidzidzi, anthu amavutika kwambiri ndi zotsatira za mavutowa. Moto utha kutentha ndi kuononga nyumba, nkhalango, mbewu ndi madambo odyetsera ziweto. Madzi osefukira atha kuyika miyoyo ya anthu pa chiopsezo ndiponso atha kukokolola nthaka yabwino ngati pamudzi palibe dongosolo lothana ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi. Madzi osefukira atha kuononga zipangizo zothandiza pa madzi akumwa ndi kuthndizira pa kafalidwe ka matenda monga kolera.
Ndondomeko izi zikupereka njira zothandiza polimbana ndi mavutowa akagwa. Ndondomekozi zikunenanso za matenda omwe amayambitsidwa ndi tizilombo tomwe timapezeka m’madzi monga likodzo, kolera ndi malungo – ndi momwe tingachizire matendawa. Ndondomekozi zikuperekanso njira zokonzeraa dongosolo lothana ndi ngozi zadzidzidzi pofuna kuonetsetsa kuti tili okonzekeratu pa mavuto ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi zamtsogolo.