Kukokoloka kwa nthaka, kudula mitengo mosasamala, njira zosayenera za ulimi, kutha kwa chonde m’nthaka, kusathana ndi kuthamanga kwa madzi a mvula pa nthaka ndi kukumbika kwa malo zimagugitsa komanso kuonongetsa malo m’Malawi muno. Kuti tichepetse kuonongeka kwa malo, tithane ndi kuonongeka kwa amalo komanso kugwiritsa ntchito malo moyenera, mutu uwu wapereka ndondomeko zochitira izi.
Chimodzi mwa zachilengedwe chomwe ndi chofunikira kwambiri ndi dothi.Dothi la chonde komanso labwino limapereka zokolola zambiri; pamene dothi loguga kapena loonongeka limapereka zokolola zochepa komanso zosadalirika.Dothi labwino limakhala ndi muyeso wabwino woti mizu ilowepo, imakhala ndi chonde, looneka bwino, limakhala ndikuthekera kosunga za moyo zambiri, komanso madzi ndipo zonsezi ndi zolumikizana. Poonetsetsa kuti dothi likhalebe labwino komanso la chonde pakufunikira njira za kasamaliridwe zosiyanasiyana monga: njira ya ulimi ya mbwezerachilengedwe, kusamalira malo odyetsera ziweto, kusamalira chonde m’nthaka, njira zopewera kukokoloka kwa nthaka, kusamalira malo okumbika, kusamalira m’mbali mwa mitsinje. Kukwaniritsa njirazi kungachepetse kuonongeka kwa chonde (makamaka kudzera mu kukokoloka kwa nthaka) ndi kuguga kwa nthaka (zomwe zimachepetsa chonde komanso kuchepetsa kasungidwe ka madzi m’dothi); kusintha kwa nyengo kungakhale kusaopsa, kulephera kwa mbewu kuchitabwino kungachepe, ndipo dothi mu gwero lonse la mtsinje lingatetezeke ndi kusungika.