A.4 Njira zopewera kukokoloka kwa nthaka ndi kuthamanga kwa madzi pa nthaka
Ndondomekozi zimapereka njira zingapo zomwe zingagwiritsidwe ntchito pa malo olimidwa ndi cholinga chofuna kuthana ndi kuthamanga kwa madzi pa nthaka. Pothana ndi kuthamanga kwa madzi pa nthaka m’minda, kukokoloka kwa nthaka kumachepa, kalowedwe ka madzi m’nthaka kamachuluka. Komanso kagwiritsidwe ntchito ka madzi kamakhala kabwino.