A.2 Kusamalira malo odyetsera ziweto
Ndondomekozi zimapereka njira zothandizira kuti zakudya za ziweto zipitirire kupezeka m’malo odyetsera ziweto uku tikusamalira ndi kutukula dothi komanso madzi- zimene ndi zofunikira ku moyo wa nyama ndi zomera. Njira zake ndi izi: kusamalira ndi kugwiritsa ntchito zinthu moyenera zimene zimakhudza zachilengedwe ndi kuonetsetsa mulingo wa kadyetsedwe ka ziweto pa malo, chiwerengero cha ziweto zodyetsedwa pamalopo ndi kagwiritsidwe ntchito ka malo. Ndondomekozi zili ndi njira zokonzeranso malo omwe adyetsedwerapo ziweto kopyola muyezo.