E.2 Umoyo

Ndondomeko za zaumoyo zikukamba kwambiri za matenda omwe amayambitsidwa ndi tizilombo tomwe timapezeka m’madzi ndi njira zosavuta kuzichita kuti inu ndi mabanja anu mukhale ndi moyo wathanzi. Njira zabwino zafotokedwa zothandiza kuti inu mukhale otetezeka ku matenda osiyanasiyana oyambitsidwa ndi tizilombo tomwe timapezeka m’madzi.  Kwenikweni uphungu waperekedwa pa momwe mungapewere ndi kuchizira matenda atatu omwe amayambitsidwa ndi tizilombo tomwe timapezeka m’madzi: malungo, likodzo ndi kolera (dziwani: ndondomeko izi sizikulowa mmalo mwa malangizo omwe a Unduna wa za Umoyo kapena dokotala amapereka). Potsiriza, njira zabwno zafotokozedwa zokhudza zomwe tingachite pa maliro, kufotokoza momwe tingachepetsere kufala kwa matenda opatsirana.