C.4 Katayidwe ka zinthu zosafunika
Zinyalala ndi zinyatsi zina zitha kuthandizira pa kufala kwa matenda ena monga malungo. Mwachitsanzo madzi a mvula omwe adikha m’mapepala a pulasitiki omwe atayidwa mwachisawawa atha kukhala malo oyenera oti udzudzu ofalitsa malungo uziswaniramo. Choncho n’kofunika kutaya zinyatsi mwadongosolo, pakhomo, kumunda ngakhalenso ku msika. Imodzi mwa njira zabwino kwambiri zotayira zinyatsi ndi kuzitenga ndi kuzigwiritsa ntchito ngati zipangizo zopangira zinthu zina zatsopano kapena kungobwereza kugwiritsanso ntchito zinthuzi monga zitini, mabotolo a galasi, mapepala, makatoni ndi mapepala a pulasitiki, ndipo zinyatsi zochokera ku zomera ndi nyama zitha kugwiritsidwa ntchito popanga manyowa a kompositi. Ndondomeko izi zikupereka malangizo opititsira patsogolo katayidwe ka zinthu zosafunika mwadongosolo.