C.2 Ukhondo

Ukhondo umapititsa patsogolo umoyo. Kukhala ndi banja, dera ndi mudzi wa anthu osadwaladwala kumathandiza kuti pakhale anthu ambiri ogwira ntchito ndikukhalanso ndi ndalama zochuluka. Ukhondo umachepetsa matenda ndi imfa. Ndondomeko izi zikupereka ndi kufotokozera njira zopititsira patsogolo ukhondo ndi kuchita zinthu mwadongosolo.