B.1 Kagwiritsidwe ntchito ka madzi mosamala ndi kugwiritsa ntchito madzi kangapo
Ndondomeko za kagwiritsidwe ntchito zikupereka uphungu womwe uthandize kutukula kasamalidwe ka madzi mu ulimi. Pogwiritsa ntchito madzi mosamala kudzera mu kusankha mbewu, kugwiritsa ntchito njira za ulimi wothirira zoyenera, komanso kugwiritsa ntchito malo ena opezeka madzi pa ulimi wothirira, zizathandiza kuti madzi azipezeka ambiri komanso kwa nthawi ndithu.