B.4 Madamu ang’onoang’ono

Ndondomekozi zikulongosola zinthu zomwe zingathandize anthu a m’mudzi kukumba madamu ang’onoang’ono kuti azisungamo madzi ochepa. Kusunga madzi kukutanthauza kuti madzi azipezeka pa gwero la madzilo kwa nthawi ndithu,kotero kuonjezera nthawi yomwe madzi angalowere pansi pa nthaka.Izi zimathandizanso kuchepetsa kusefukira kwa madzi m’mitsinje, ndipo zimathandiza kuti madzi omwe akanaonongeka agwiritsidwe ntchito bwino.