Mavuto ogwa mwadzidzidzi ndi ngozi zitha kuchitika pena paliponse komanso nthawi ina iliyonse. Komabe m’madera momwe zachilengedwe zaonongeka kapena momwe malibe dongosolo lokhudza mavuto ogwa mwadzidzidzi, anthu amavutika kwambiri ndi zotsatira za mavutowa. Moto utha kutentha ndi kuononga nyumba, nkhalango, mbewu ndi madambo odyetsera ziweto. Madzi osefukira atha kuyika miyoyo ya anthu pa chiopsezo ndiponso atha kukokolola nthaka yabwino ngati pamudzi palibe dongosolo lothana ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi. Madzi osefukira atha kuononga zipangizo zothandiza pa madzi akumwa ndi kuthndizira pa kafalidwe ka matenda monga kolera.

Ndondomeko izi zikupereka njira zothandiza polimbana ndi mavutowa akagwa. Ndondomekozi zikunenanso za matenda omwe amayambitsidwa ndi tizilombo tomwe timapezeka m’madzi monga likodzo, kolera ndi malungo – ndi momwe tingachizire matendawa. Ndondomekozi zikuperekanso njira zokonzeraa dongosolo lothana ndi ngozi zadzidzidzi pofuna kuonetsetsa kuti tili okonzekeratu pa mavuto ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi zamtsogolo.